3
1 Usiku wonse ndili pa bedi langa
ndinafunafuna amene mtima wanga umamukonda;
ndinamufunafuna koma osamupeza.
2 Ndikudzuka tsopano ndipo ndidzayendayenda mu mzinda,
mʼmisewu yake ndi mʼmabwalo ake;
ndidzamufunafuna amene mtima wanga umamukonda.
Kotero ine ndinamufunafuna iyeyo koma osamupeza.
3 Alonda anandipeza
pamene ankayendera mzinda.
“Kodi mwamuonako amene mtima wanga umamukonda?”
4 Nditawapitirira pangʼono
ndinamupeza amene mtima wanga umamukonda.
Ndinamugwira ndipo sindinamulole kuti achoke
mpaka nditamulowetsa mʼnyumba ya amayi anga,
mʼchipinda cha amene anandibereka.
5 Inu akazi a ku Yerusalemu, ndithu ndikukupemphani
pali gwape ndi mbawala yayikazi zakuthengo:
Musachigwedeze chikondi kapena kuchiutsa
mpaka pamene chifunire ichocho.
6 Kodi ndani amene akubwera kuchokera ku chipululu
ngati utsi watolotolo,
wonunkhira mure ndi lubani,
zopangidwa kuchokera ku zonunkhira zonse za anthu amalonda?
7 Ona! Chimenecho ndi chonyamulira Solomoni,
choperekezedwa ndi asilikali 60,
anthu amphamvu a ku Israeli,
8 onse atanyamula lupanga,
onse odziwa bwino nkhondo,
aliyense ali ndi lupanga pambali pake,
kukonzekera zoopsa za usiku.
9 Mfumu Solomoni anadzipangira chonyamulirachi;
anachipanga ndi matabwa ochokera ku Lebanoni.
10 Milongoti yake anayipanga yasiliva,
kumbuyo kwake kwa golide.
Mipando yake inakutidwa ndi nsalu yapepo,
anakongoletsa mʼkati mwake ndi chikondi
cha akazi a ku Yerusalemu.
11 Tukulani inu akazi a ku Ziyoni
ndipo mudzaone mfumu Solomoni atavala chipewa chaufumu,
chipewa chaufumu chimene amayi ake anamuveka
pa tsiku la ukwati wake,
tsiku limene mtima wake unasangalala.