16
“Ine ndakuwuzani zonsezi kuti musadzakhumudwe. Iwo adzakuchotsani mʼsunagoge mwawo. Kunena zoona, nthawi ikubwera imene aliyense amene adzakuphani adzaganiza kuti akutumikira Mulungu. Iwo adzachita zoterozo chifukwa sanadziwe Atate kapena Inenso. Ine ndakuwuzani izi kuti nthawi ikadzafika mudzakumbukire kuti Ine ndinakuchenjezani kale. Ine sindinakuwuzeni izi poyamba paja chifukwa ndinali nanu.”
Ntchito ya Mzimu Woyera
“Tsopano Ine ndikupita kwa Iye amene anandituma koma palibe wina mwa inu akundifunsa kuti, ‘Kodi mukupita kuti?’ Muli ndi chisoni kwambiri chifukwa ndakuwuzani zimene. Komatu ndakuwuzani zoona. Ine ndikuti kuli bwino kwa inu kuti ndichoke. Ngati sindichoka, Nkhosweyo sidzabwera kwa inu, koma ngati Ine ndipita, ndidzamutumiza kwa inu. Iye akabwera, adzatsutsa dziko lapansi za uchimo, zachilungamo ndi zachiweruzo. Za uchimo, chifukwa anthu sakhulupirira Ine. 10  Za chilungamo, chifukwa Ine ndi kupita kwa Atate, kumene simudzandionanso. 11  Za chiweruzo, chifukwa wolamulira dziko lino lapansi waweruzidwa tsopano.
12  “Ine ndili ndi zambiri zoti ndiyankhule nanu, koma simungathe kuzilandira tsopano. 13  Koma pamene Iye, Mzimu wachoonadi, abwera, adzakutsogolerani mʼchoonadi chonse. Iye sadzayankhula mwa Iye yekha, adzayankhula zokhazo zimene wamva ndipo Iye adzakuwuzani zimene zikubwera. 14  Iye adzalemekeza Ine chifukwa adzatenga za Ine nadzakudziwitsani. 15  Zonse za Atate ndi zanga. Ichi nʼchifukwa chake Ine ndanena kuti Mzimu Woyera adzatenga kwa Ine zanga kuti muzidziwe.”
Chisoni cha Ophunzira Chisandulika Chimwemwe
16 Yesu anapitiriza kuyankhula kuti, “Mwa kanthawi kochepa, simudzandionanso, ndipo patatha nthawi pangʼono mudzandionanso.”
17 Ena a ophunzira ake anati kwa wina ndi mnzake, “Kodi Iye akutanthauza chiyani ponena kuti, ‘Mwa kanthawi kochepa, simudzandionanso,’ ndi ‘ndipo patatha nthawi pangʼono mudzandionanso,’ ndiponso ‘chifukwa ndikupita kwa Atate?’ ” 18 Iwo anapitiriza kufunsana kuti, “Kodi akutanthauza chiyani, ‘kanthawi kochepa?’ Ife sitikumvetsetsa chimene Iye akuyankhula.”
19 Yesu anadziwa kuti ankafuna kuti amufunse za zimenezi, choncho anawafunsa kuti, “Kodi mukufunsana wina ndi mnzake chimene Ine ndimatanthauza pamene ndinati, ‘Mwa kanthawi kochepa simudzandionanso,’ ndi ‘patatha nthawi pangʼono mudzandionanso?’ 20  Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti inu mudzalira ndi kubuma pomwe dziko lapansi lidzakhale likukondwera. Inu mudzamva chisoni, koma chisoni chanu chidzasandulika chimwemwe. 21  Mayi akamabereka mwana amamva ululu chifukwa nthawi yake yafika; koma mwana wake akabadwa amayiwala ululu wake chifukwa cha chimwemwe chake chakuti mwana wabadwa mʼdziko lapansi. 22  Chimodzimodzinso ndi inu. Tsopano ino ndi nthawi yanu yomva chisoni, koma Ine ndidzakuonaninso ndipo inu mudzasangalala, ndipo palibe amene adzachotsa chimwemwe chanu. 23  Tsiku limenelo inu simudzandipemphanso kalikonse. Ine ndikukuwuzani zoona kuti Atate anga adzakupatsani chilichonse chimene mudzapempha mʼdzina langa. 24  Mpaka tsopano simunapemphe kalikonse mʼdzina langa. Pemphani ndipo mudzalandira, ndipo chimwemwe chanu chidzakhala chathunthu.
25  “Ngakhale ndakhala ndikuyankhula mʼmafanizo, nthawi ikubwera imene Ine sindidzagwiritsanso ntchito mafanizo otere koma ndidzakuwuzani momveka za Atate anga. 26  Tsiku limenelo inu mudzapempha mʼdzina langa. Ine sindikunena kuti ndidzapempha Atate mʼmalo mwanu ayi. 27  Atate mwini anakukondani chifukwa inu mwandikonda Ine ndipo mwakhulupirira kuti Ine ndinabwera kuchokera kwa Atate. 28  Ine ndinabwera kuchokera kwa Atate ndi kulowa mʼdziko lapansi. Tsopano ndikulisiya dziko lapansi kubwerera kwa Atate.”
29 Kenaka ophunzira ake anati, “Tsopano mukuyankhula momveka bwino ndi mopanda mafanizo. 30 Tsopano ife tikuona kuti Inu mumadziwa zinthu zonse ndi kuti sipafunika wina aliyense kukufunsani. Mwa ichi ife takhulupirira kuti Inu munachokera kwa Mulungu.”
31 Yesu anawafunsa kuti, “Kodi tsopano mwakhulupirira?” 32  Koma nthawi ikubwera ndipo yafika, pamene inu mudzabalalitsidwa, aliyense ku nyumba yake. Inu mudzandisiya ndekhandekha. Koma Ine sindili ndekha, pakuti Atate anga ali nane.
33  “Ine ndakuwuzani izi kuti mwa Ine mukhale nawo mtendere. Mʼdziko lapansi mudzakhala nawo mavuto. Koma limbikani mtima! Ine ndaligonjetsa dziko lapansi.”