Habakuku
1
1 Uthenga umene mneneri Habakuku analandira mʼmasomphenya.
Dandawulo la Habakuku
2 Kodi inu Yehova, ndidzakhala ndikukupemphani thandizo kwa nthawi yayitali motani,
koma wosayankha?
Kapena kufuwulira kwa inu kuti, “Chiwawa kuno!”
koma wosatipulumutsa?
3 Chifukwa chiyani mukundionetsa zinthu zoyipa?
Chifukwa chiyani mukundionetsa mavutowa?
Ndikuona chiwonongeko ndi chiwawa;
pali ndewu ndi kukangana kwambiri.
4 Kotero malamulo anu atha mphamvu,
ndipo chilungamo sichikugwira ntchito.
Anthu oyipa aposa olungama,
kotero apotoza chilungamo.
Yankho la Yehova
5 “Yangʼanani pakati pa mitundu ya anthu, ndipo penyetsetsani,
ndipo muthedwe nazo nzeru.
Pakuti ndidzachitadi zinthu pa nthawi yanu
zimene inu simudzazikhulupirira,
ngakhale wina atakufotokozerani.
6 Pakuti taonani, Ine ndikuwutsa Ababuloni,
anthu ankhanza ndiponso amphamvu,
amene amapita pa dziko lonse lapansi
kukalanda malo amene si awo.
7 Iwowa ndi anthu ochititsa mantha, ndipo ndi owopsa;
amadzipangira okha malamulo
ndi kudzipezera okha ulemu.
8 Akavalo awo ndi aliwiro kwambiri kupambana akambuku
ndi owopsa kupambana mimbulu yolusa nthawi ya madzulo.
Okwerapo awo akuthamanga molunjika;
a pa akavalo awo ndi ochokera kutali,
akuwuluka ngati chiwombankhanga chofuna kugwira nyama;
9 onse akubwera atakonzekera zachiwawa.
Gulu la ankhondo likubwera ngati mphepo ya mʼchipululu
ndi kugwira akapolo ochuluka ngati mchenga.
10 Akunyoza mafumu
ndiponso kuchitira chipongwe olamulira.
Akupeputsa mizinda yonse yotetezedwa;
akumanga mitumbira ndi kulanda mizindayo.
11 Kenaka amasesa mofulumira ngati mphepo nʼkumangopitirirabe,
anthu ochimwa, amene mphamvu zawo ndiye mulungu wawo.”
Dandawulo Lachiwiri la Habakuku
12 Inu Yehova, kodi sindinu wachikhalire?
Mulungu wanga, Woyera wanga, ife sitidzafa.
Inu Yehova, munawasankha anthuwo kuti abweretse chiweruzo;
Inu Thanthwe, munawayika iwowo kuti atilange.
13 Maso anu ndi oyera kwambiri safuna kuona choyipa;
Inu simulekerera cholakwa.
Chifukwa chiyani nanga mukulekerera anthu ochita zachinyengowa?
Chifukwa chiyani muli chete pamene anthu oyipa
akuwononga anthu olungama kupambana iwowo?
14 Mwasandutsa anthu kukhala ngati nsomba zamʼnyanja,
ngati zolengedwa zamʼnyanja zimene zilibe wolamulira.
15 Mdani wawo woyipa amakoka anthu onse ndi mbedza,
amawakola mu ukonde wake,
amawasonkhanitsa mu khoka lake;
kotero iyeyo amakondwa ndi kusangalala.
16 Choncho iye amaperekera nsembe ukonde wake
ndiponso kufukizira lubani khoka lake,
popeza ukonde wakewo ndiye umamubweretsera moyo wapamwamba
ndipo amadya chakudya chabwino kwambiri.
17 Kodi iye azipitirabe kugwiritsa ntchito makoka akewo,
kuwononga mitundu ya anthu mopanda chifundo?