3
Kuwukira kwa Mowabu
Yoramu mwana wa Ahabu anakhala mfumu ya Israeli ku Samariya mʼchaka cha 18 cha Yehosafati mfumu ya ku Yuda ndipo analamulira zaka khumi ndi ziwiri. Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova koma sizinafanane ndi zimene anachita abambo ndi amayi ake. Iye anachotsa fano la mwala la Baala limene abambo ake anapanga. Komabe anawumirira kuchita machimo a Yeroboamu mwana wa Nebati, amene anachimwitsa nawo Israeli ndipo sanafune kuwaleka.
Tsono Mesa, mfumu ya ku Mowabu ankaweta nkhosa, ndipo iye ankayenera kumapereka kwa mfumu ya ku Israeli chaka ndi chaka ana ankhosa onenepa okwanira 100,000 pamodzi ndi ubweya wankhosa 100,000 zazimuna. Koma atamwalira Ahabu, mfumu ya ku Mowabu inawukira mfumu ya ku Israeli. Choncho nthawi imeneyi mfumu Yoramu inatuluka mu Samariya ndi kukasonkhanitsa Aisraeli onse. Yoramu anatumizanso uthenga uwu kwa Yehosafati mfumu ya ku Yuda: “Mfumu ya ku Mowabu yandiwukira. Kodi ungapite nane kukamenyana ndi Mowabu?”
Iye anayankha kuti, “Ine ndidzapita nawe. Iwe ndi ine ndife anthu amodzi, anthu anga ali ngati anthu ako, akavalo anga ali ngati akavalo ako.”
Yehosafati anafunsa kuti, “Kodi tidzera njira iti popita ku nkhondoko?”
Yoramu anayankha kuti, “Tidzera ku Chipululu cha Edomu.”
Choncho mfumu ya ku Israeli inanyamuka pamodzi ndi mfumu ya ku Yuda ndi ya ku Edomu. Ndipo atayenda mozungulira mʼchipululu kwa masiku asanu ndi awiri, asilikali analibe madzi woti amwe kapena kumwetsa nyama zawo zosenza katundu.
10 Mfumu inafuwula kuti, “Nʼchiyani chomwe chikutichitikira! Kodi Yehova wasonkhanitsa mafumu atatu pamodzi kuti atipereke mʼmanja mwa Amowabu?”
11 Koma mfumu Yehosafati inafunsa kuti, “Kodi kuno kulibe mneneri wa Yehova woti tingakafunse kwa Yehova kudzera mwa iyeyo?”
Mtsogoleri wa ankhondo wa mfumu ya ku Israeli anayankha kuti, “Alipo, Elisa mwana wa Safati. Iye anali mtumiki wa Eliya.”
12 Yehosafati anati, “Yehova amayankhula kudzera mwa iye.” Choncho mfumu ya ku Israeli pamodzi ndi Yehosafati ndiponso mfumu ya ku Edomu anapita kwa Elisa.
13 Elisa ananena kwa mfumu ya ku Israeli kuti, “Pali ubale wanji pakati pa inu ndi ine? Pitani kwa aneneri a abambo ndi amayi anu.”
Mfumu ya ku Israeli inayankha kuti, “Ayi, pakuti ndi Yehova amene anatisonkhanitsa ife mafumu atatu pamodzi kuti atipereke mʼmanja mwa Amowabu.”
14 Elisa anati, “Pali Yehova Wamphamvuzonse amene ndimamutumikira, pakanapanda kuti ndimamuchitira ulemu Yehosafati mfumu ya ku Yuda, sindikanakulabadirani kapena kukuyangʼanani nʼkomwe. 15 Koma tsopano ndiyitanireni munthu wodziwa kuyimba bwino zeze.”
Munthuyo akuyimba zeze, mphamvu ya Yehova inafika pa Elisa, 16 ndipo anati, “Yehova akuti, ‘Kumbani ngalande mʼchigwa chonse.’ 17 Pakuti Yehova akunena kuti, ‘Simudzaona mphepo kapena mvula, komabe chigwa ichi chopanda madzi chidzadzaza ndi madzi, ndipo inu mudzamwa pamodzi ndi ngʼombe zanu ndiponso nyama zanu zonse.’ 18 Izi ndi zosavuta pamaso pa Yehova. Ndipo adzaperekanso Amowabu mʼmanja mwanu. 19 Mudzagonjetsa mizinda yawo yonse yotetezedwa ndiponso mizinda yawo ikuluikulu. Mudzagwetsa mtengo wabwino uliwonse, mudzatseka akasupe onse amadzi, ndiponso mudzawononga minda yawo yonse yachonde poponyamo miyala.”
20 Mmawa mwake, nthawi yopereka nsembe ili pafupi, anangoona madzi akutuluka kuchokera ku Edomu, ndipo malo onse anadzaza ndi madzi.
21 Tsono nʼkuti Amowabu onse atamva kuti mafumu abwera kudzachita nawo nkhondo. Kotero, anayitana munthu aliyense, wamkulu ndi wamngʼono amene ankatha kugwira chida chankhondo ndipo anakayima ku malire a dziko lawo. 22 Amowabu atadzuka mmamawa, dzuwa likuwala pa madziwo, anaona madziwo akuoneka wofiira ngati magazi patsogolo pawo. 23 Ndipo iwo anati, “Taonani magazi! Mafumu aja amenyana okhaokha ndipo aphana. Amowabu, tsopano ndi nthawi yofunkha!”
24 Koma Amowabu atafika ku misasa ya Israeli, Aisraeli ananyamuka ndi kumenyana nawo mpaka anathawa. Ndipo Aisraeli analowa mʼdzikolo ndi kupha Amowabu. 25 Aisraeli anagumula mizinda yawo ndipo munthu aliyense anaponya mwala pa munda uliwonse wachonde mpaka utadzaza ndi miyala. Iwo anatseka akasupe onse amadzi ndiponso anadula mtengo wabwino uliwonse. Mzinda wa Kiri Hareseti wokha ndiye unatsala wotetezedwa koma anthu oponya miyala anawuzungulira nawuthiranso nkhondo.
26 Mfumu ya ku Mowabu itaona kuti nkhondo ikumulaka, inatenga anthu 700 a malupanga kuti athawe modutsa mfumu ya ku Edomu, koma inalephera. 27 Choncho inatenga mwana wake wamwamuna woyamba kubadwa, amene akanalowa ufumu mʼmalo mwake, ndi kumupereka nsembe pa khoma la mzinda. Zimenezi zinachititsa kuti mkwiyo ndi ukali wa Amowabu ukule kwambiri pa Aisraeli ndipo Aisraeliwo anathawa nabwerera ku dziko la kwawo.